10 Ndodo yacifumu siidzacoka mwa Yuda,Kapena wolamulira pakati pa mapazi ace,Kufikira atadza Silo;Ndipo anthu adzamvera iye.
11 Adamanga mwana wa kavalo wace pampesa,Ndi mwana wa buru wace pa mpesa wosankhika;Natsuka malaya ace m'vinyo,Ndi copfunda cace m'mwazi wa mphesa.
12 Maso ace adzafiira ndi vinyo,Ndipo mana ace adzayera ndi mkaka.
13 Zebuloni adzakhala m'doko la kunyanja;Ndipo iye adzakhala doko la ngalawa;Ndipo malire ace adakhala pa Zidoni.
14 Isakara ndiye buru wolimba,Alinkugona pakati pa makola;
15 Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino,Ndi dziko kuti linali lokondweretsa;Ndipo anaweramitsa phewa lace kuti anyamule,Nakhala kapolo wakugwira nchito ya msonkho,
16 Dani adzaweruza anthu ace,Monga limodzi la mafuko a Israyeli.