8 Yuda, abale ako adzakuyamika iwe;Dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako;Ana amuna a atate wako adzakuweramira.
9 Yuda ndi mwana wa mkango,Kucokera kuzomotola, mwananga, wakwera;Anawerama pansi, anabwatama ngati mkango,Ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?
10 Ndodo yacifumu siidzacoka mwa Yuda,Kapena wolamulira pakati pa mapazi ace,Kufikira atadza Silo;Ndipo anthu adzamvera iye.
11 Adamanga mwana wa kavalo wace pampesa,Ndi mwana wa buru wace pa mpesa wosankhika;Natsuka malaya ace m'vinyo,Ndi copfunda cace m'mwazi wa mphesa.
12 Maso ace adzafiira ndi vinyo,Ndipo mana ace adzayera ndi mkaka.
13 Zebuloni adzakhala m'doko la kunyanja;Ndipo iye adzakhala doko la ngalawa;Ndipo malire ace adakhala pa Zidoni.
14 Isakara ndiye buru wolimba,Alinkugona pakati pa makola;