1 Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'cifanizo ca Mulungu;
2 anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo nacha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.
3 Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'cifanizo cace; namucha dzina lace Seti.
4 Masiku ace Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana amuna ndi akazi.
5 Masiku ace onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.
6 Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi;