1 Ndipo Yosefe anagwapa nkhope ya atate wace, namlirira iye nampsompsona iye.
2 Ndipo Yosefe anauza akapolo ace asing'anga kutiakonze atate wace: ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israyeli.
3 Ndipo anatha masiku ace makumi anai a iye; cifukwa comweco amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aaigupto anamlira iye masiki makumi asanu ndi awiri.
4 Atapita masiku akumlira iye Yosefe anati kwa mbumba ya Farao kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamase panu, nenanitu m'makutu a Parae kuti,
5 Atate wanga anandilumbi ritsa ine, kuti, Taona, ndirinkufa m'manda m'mene ndadzikonzeran ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundi loletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabwe ranso.
6 Ndipo Farao anati, Pita kaike atate wako, monga iye anaku lumbiritsa iwe.