17 Muziti cotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kucimwa kwao, cifukwa kuti anakucitirani inu coipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa aka polo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.
18 Ndiponso abale ace anamuka namgwadira pamaso pace; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.
19 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndiri ine kodi m'malo a Mulungu?
20 Koma inu, munandipangira ine coipa; koma Mulungu anacipangira cabwino, kuti kucitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri,
21 Ndipo tsopano musaope; Ine ndidzacereza inu, ndi ana anu ang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.
22 Ndipo Yosefe anakhala m'Aigupto, iye, ndi mbumba ya atate wace; ndipo Yosefe anakhala ndi movo zaka zana limodzi ndi khumi.
23 Ndipo Yosefe anaona ana a Efraimu a mbadwo wacitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.