5 Atate wanga anandilumbi ritsa ine, kuti, Taona, ndirinkufa m'manda m'mene ndadzikonzeran ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundi loletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabwe ranso.
6 Ndipo Farao anati, Pita kaike atate wako, monga iye anaku lumbiritsa iwe.
7 Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wace; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akuru a pa mbumba yace, ndi akuru onse a m'dziko la Aigupto,
8 ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ace, ndi mbumba ya atate wace: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni.
9 Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magareta ndi apakavalo; ndipo panali khamc lalikuru.
10 Ndipo anafika pa dwale la Atadi, liri tsidya lija la Yordano, pamenepo anamlira maliro a atate wace masiku asanu ndi limodzi.
11 Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo; Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akuru a Aaigupto: cifukwa cace dzina la pamenepo linachedwa Abeli-mizraimu, pali tsidya lija la Yordano.