1 Ndipo panali pamene anthu anayamba kucuruka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo,
2 kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
3 Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, cifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ace adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.
4 Pa dziko lapansi panali anthu akurukuru masiku omwewo ndiponso pambuyo pace, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.
5 Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukuru pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.
6 Ndipo Yehova anamva cisoni cifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anabvutika m'mtima mwace.
7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva cisoni cifukwa ndapanga izo.