3 Ndiposo mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi.
4 Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzabvumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga pa dziko lapansi,
5 Ndipo anacita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.
6 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene cigumula ca madzi cinali pa dziko lapansi.
7 Ndipo analowa Nowa ndi ana ace ndi mkazi wace ndi akazi a ana ace m'cingalawamo, cifukwa ca madzi a cigumula.
8 Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,
9 zinalowa ziwiri ziwiri kwa Nowa m'cingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.