23 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? tsopano udzapenya ngati mau anga adzakucitikira kapena iai.
24 Ndipo Mose anaturuka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akuru a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa cihema.
25 Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena nave, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akuru makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.
26 Koma amuna awiri anatsalira m'cigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzace ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanaturuka kumka kucihema; ndipo ananenera m'cigono.
27 Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'cigono.
28 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wace, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.
29 Koma Mose anati kwa iye, Kodi ucita nsanje nao cifukwa ca ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri! mwenzi Yehova atawaikira mzimu wace!