1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
2 Ili ndi lemba la cilamulo Yehova adalamuliraci, ndi kuti, Nena ndi ana a Israyeli kuti azikutengera ng'ombe ramsoti yofiira, yangwiro yopanda enema, yosamanga m'goli;
3 ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naiturutse iye kunja kwa cigono, ndipo wina aiphe pamaso pace.
4 Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wace ndi cala cace, nawazeko mwazi wace kasanu ndi kawiri pakhomo pa cihema cokomanako.
5 Pamenepo atenthe ng'ombe yamsotiyo pamaso pace; atenthe cikopa cace ndi nyama yace, ndi mwazi wace, pamodzi ndi cipwidza cace.
6 Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa mota irikupsererapo ng'ombe yamsoti.
7 Pamenepo wansembe atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi; ndipo atatero alowenso kucigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.