1 Ndipo ana a Israyeli, ndilo khamu lonse, analowa m'cipululu ca Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriamu, naikidwakomweko.
2 Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni.
3 Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!
4 Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'cipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?
5 Ndipo munatikwezeranji kutiturutsa m'Aigupto, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.
6 Ndipo Mose ndi Aroni anacoka pamaso pa msonkhano kumka ku khomo la cihema cokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.