20 Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anaturukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.
21 Potero Edomu anakana kulola Israyeli kupitira pa malire ace; cifukwa cace Aisrayeli anampatukira.
22 Ndipo anayenda ulendo kucokera ku Kadesi; ndi ana a Israyeli, ndilo khamu lonse, anadza ku phiri la Hori.
23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti,
24 Aroni adzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israyeli, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.
25 Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wace, nukwere nao m'phiri la Hori;
26 nubvule Aroni zobvala zace, numbveke Eleazara mwana wace; ndipo Aroni adzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace, nadzafa komweko.