8 Mulungu amturutsa m'Aigupto;Ali nayo mphamvu yonga ya njati;Adzawadya amitundu, ndiwo adani ace.Nadzaphwanya mafupa ao, Ndi kuwapyoza ndi mibvi yace.
9 Anaunthama, nagona pansi ngati mkango,Ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani?Wodalitsika ali yense wakudalitsa iwe,Wotemberereka ali yense wakutemberera iwe.
10 Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani ansa, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.
11 Cifukwa cace thawira ku malo ako tsopano; ndikadakucitira ulemu waukuru; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.
12 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,
13 Cinkana Balaki akandipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kucita cokoma kapena coipa ine mwini wace; conena Yehova ndico ndidzanena ine?
14 Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzacitira anthu anu, masiku otsiriza.