2 popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.
3 Pamene Israyeli anaphatikana ndi Baala Peori, Mulungu anapsa mtima pa Israyeli.
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akuru onse a anthu nuwapacikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova ucoke kwa Israyeli.
5 Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israyeli, Iphani, yense anthu ace adapatikanawo ndi Baala-Peori.
6 Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israyeli, nabwera naye mkazi Mmidyani kudza naye kwa abale ace, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israyeli, pakulira iwo pa khomo la cihema cokomanako.
7 Pamene Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anaciona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lace;
8 natsata munthu M-israyeli m'hema, nawamoza onse awiri, munthu M-israyeli ndi mkaziyo m'mimba mwace. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israyeli.