5 Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israyeli, Iphani, yense anthu ace adapatikanawo ndi Baala-Peori.
6 Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israyeli, nabwera naye mkazi Mmidyani kudza naye kwa abale ace, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israyeli, pakulira iwo pa khomo la cihema cokomanako.
7 Pamene Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anaciona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lace;
8 natsata munthu M-israyeli m'hema, nawamoza onse awiri, munthu M-israyeli ndi mkaziyo m'mimba mwace. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israyeli.
9 Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.
10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
11 Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israyeli, popeza anacita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israyeli m'nsanje yanga.