12 Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwace, nadze nayo nkhosa yamphongo ya caka cimodzi ikhale nsembe yoparamula; koma masiku adapitawa azikhala cabe, popeza anadetsa kusala kwace.
13 Ndipo cilamulo ca Mnaziri, atatha masiku a kusala kwace ndi ici: azidza naye ku khomo la cihema cokomanako;
14 pamenepo abwere naco copereka cace kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya caka cimodzi yopanda cirema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yamsoti yopanda cirema ikhale nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda cirema ikhale nsembe yoyamika;
15 ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.
16 Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yace yaucimo, ndi nsembe yace yopsereza;
17 naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.
18 Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wace wa kusala kwace pa khomo la cihema cokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wace wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.