1 NDIPO kunali caka ca makumi atatu, mwezi wacinai, tsiku lacisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.
2 Tsiku lacisanu la mwezi, ndico caka cacisanu ca kutengedwa ndende mfumu Yoyakini,
3 anadzadi mau a Yehova kwa Ezekieli wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Akasidi kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.
4 Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wocokera kumpoto, mtambo waukuru ndi moto wopfukusika m'mwemo, ndi pozungulira pace padacita ceza, ndi m'kati mwace mudaoneka ngati citsulo cakupsa m'kati mwa moto.
5 Ndi m'kati mwace mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,
6 ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.