41 Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kucita cigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yacigololo.
42 M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakucokera, ndipo ndidzakhala cete wosakwiyanso.
43 Popeza sunakumbukila masiku a ubwana wako, koma wandibvuta nazo zonsezi, cifukwa cace taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzacita coipa ici coonjezerapo pa zonyansa zako zonse.
44 Taona, ali yense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga mace momwemo mwana wace.
45 Iwe ndiwe mwana wa mako wonyansidwa naye mwamuna wace ndi ana ace, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Mhiti, ndi atate wako ndiye M-amori.
46 Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala ku dzanja lako lamanzere, iye ndi ana ace akazi; ndi mng'ono wako wokhala ku dzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ace akazi.
47 Koma sunayenda m'njira zao, kapena kucita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kubvunda kwako, m'njira zako zonse.