7 Ndipo ukanene nao mau anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka.
8 Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ici ndirikunena nawe; usakhale iwewopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye comwe ndikupatsa.
9 Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londiturutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo;
10 naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi cisoni, ndi tsoka.