2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israyeli kulitsutsa;
3 nuziti kwa dziko la Israyeli, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'cimace, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.
4 Popeza ndidzakulikhira olungama ndi oipa, cifukwa cace lupanga langa lidzasololokera anthu onse, kuyambira kumwera kufikira kumpoto;
5 ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupangalanga m'cimace, silidzabwereranso.
6 Koma wobadwa ndi munthu iwe, usa moyo, ndi kuduka msana, ndi kuwawa mtima, uuse moyo pamaso pao.
7 Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo cifukwa ninji? uzikati, Cifukwa ca mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uli wonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uli wonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona irinkudza, inde idzacitika, ati Ambuye Yehova.
8 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,