22 Monga siliva asungunuka m'kati mwa ng'anjo, momwemo inu mudzasungunuka m'kati mwace; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga.
23 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,
24 Wobadwa ndi munthu iwe, nena ndi Yuda, Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, losabvumbwa mvula tsiku la ukalilo.
25 Pali ciwembu ca aneneri ace pakati pace, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda cuma ndi za mtengo wace, acurukitsa amasiye pakati pace.
26 Ansembe ace acitira coipa cilamulo canga, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zosapatulika, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.
27 Akalonga ace m'kati mwace akunga afisi akumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.
28 Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pace, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova posanena Yehova.