4 Ndipo adzagumula malinga a Turo, ndi kugwetsa nsanja zace; inde ndidzausesa pfumbi lace, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.
5 Udzakhala poyanika khokapakati pa nyanja, pakuti Ine ndacinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala cofunkha ca amitundu.
6 Ndi ana ace akazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Turo Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mfumu ya mafumu, yocokera kumpoto ndi akavalo, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.
8 Ana ako akazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira cikopa.
9 Nadzaikira malinga ako zogumulira, nadzagwetsa nsanja zako ndi zida zace.
10 Papeza acuruka akavalo ace, pfumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magareta, palowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mudzi popasukira linga lace.