1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Turo nyimbo ya maliro;
3 nuti kwa Turo, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakucita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Turo, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.
4 M'mphepete mwako muli m'kati mwa nyanja, iwo anakumanga iwe anakonza kukongola kwako kukhale kwangwiro.
5 Anaceka matabwa ako onse amlombwa wa ku Seniri, anatenga mikungudza ya ku Lebano kukupangira milongoti.