7 cifukwa cace taona, ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.
8 Adzakutsitsira kumanda, nudzafa mafedwe a ophedwa m'kati mwa nyanja.
9 Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.
10 Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.
11 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,
12 Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Turo, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi cizindikilo, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.
13 Unali m'Edene, munda wa Mulungu, mwala uli wonse wa mtengo wace unali copfunda cako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golidi; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.