9 Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.
10 Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.
11 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,
12 Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Turo, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi cizindikilo, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.
13 Unali m'Edene, munda wa Mulungu, mwala uli wonse wa mtengo wace unali copfunda cako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golidi; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.
14 Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.
15 Unali wangwiro m'njira zako cilengedwere iwe, mpaka cinapezeka mwa iwe cosalungama.