9 Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zace zocuruka; ndi mitengo yonse ya m'Edene inali m'munda wa Mulungu inacita nao nsanje.
10 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wace, nufikitsa nsonga yace kumitambo, nukwezeka mtima wace m'kukula kwace,
11 ndidzaupereka m'dzanja la wamphamvu wa amitundu; iye adzacita naotu, Ine ndautaya mwa coipa cace.
12 Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zace zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zace zinatyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika ku mthunzi wace, niusiya.
13 Pogwera pace padzakhala mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi nyama zonse za kuthengo zidzakhala pa nthambi zace;
14 kuti mitengo iri yonse ya kumadzi isadzikuze cifukwa ca msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa ku imfa munsi mwace mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.
15 Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinacititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinacepsa mitsinje yace, ndi madzi akuru analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebano, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota cifukwa ca uwo.