19 Ndipo woipa akabwerera kuleka coipa cace, nakacita coyenera ndi colungama, adzakhala ndi moyo nazo.
20 Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israyeli inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zace.
21 Ndipo kunali caka cakhumi ndi ciwiri ca undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lacisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi.
22 Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.
23 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
24 Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala ku mabwinja a dziko la Israyeli anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko colowa cace; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife colowa cathu.
25 Cifukwa cace unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu ku mafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?