2 Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israyeli; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israyeli odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?
3 Mukudya mafuta, mubvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa.
4 Zofoka simunazilimbitsa; yodwala simunaiciritsa, yotyoka simunailukira chika, yopitikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa,
5 M'mwemo zinamwazika posowa mbusa, nizinakhala cakudya ca zirombo ziri zonse za kuthengo, popeza zinamwazika.
6 Nkhosa zanga zinasokera ku mapiri ali onse, ndi pa citunda ciri conse cacitali; inde nkhosa zanga zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.
7 Cifukwa cace abusa inu, imvani mau a Yehova:
8 Pali ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala cakudya ca zirombo zonse za kuthengo, cifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafuna nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;