16 Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israyeli anzace; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efraimu, ndi wa nyumba yonse ya Israyeli anzace;
17 nuiphatikize wina ndi unzace ikhale mtengo umodzi m'dzanja lako.
18 Ndipo ana a anthu amtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi?
19 unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efraimu, ndi wa mafuko a Israyeli anzace, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.
20 Ndipo mitengo imene ulembapo idzakhala m'dzanja mwako pamaso pao.
21 Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israyeli pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa ku mbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;
22 ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israyeli; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.