14 Cifukwa cace nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israyeli, sudzacidziwa kodi?
15 Ndipo udzaturuka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukuru ndi nkhondo yaikuru;
16 ndipo udzakwerera anthu anga Israyeli ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzacitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.
17 Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israyeli, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?
18 Ndipo kudzacitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israyeli, ati Ambuye Yehova, ukali wanga udzakwera m'mphuno mwanga.
19 Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukuru m'dziko la Israyeli;
20 motero kuti nsomba za m'nyanja, ndi mbalame za m'mlengalenga, ndi nyama za kuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi.