7 Ukonzekeretu, Inde udzikonzeretu, iwe ndi msonkhano wako wonse unakusonkhanira, nukhale iwe mtsogoleri wao.
8 Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituruke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israyeli, amene adakhala acipululu cikhalire; koma liturutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.
9 Ndipo udzakwera udzadza ngati mkuntho, udzanga mtambo kuphimba dziko, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.
10 Atero Ambuye Yehova, Kudzacitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira ciwembu coipa,
11 nudzati, Ndidzakwera kumka ku dziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mipingiridzo, kapena zitseko;
12 kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoweta ndi cuma, okhala pakati pa dziko.
13 Seba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisi, ndi misona yace yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kucoka nazo siliva ndi golidi, kucoka nazo zoweta ndi cuma, kulanda zankhondo zambiri?