11 Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda m'Israyeli, cigwa ca opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wace wonse, nadzacicha, Cigwa ca unyinji wa Gogi.
12 Ndi a nyumba ya Israyeli adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.
13 Inde anthu onse a m'dziko adzawaika, nadzamveka nako tsiku lakulemekezedwa Ine, ati Ambuye Yehova.
14 Ndipo adzasankha anthu akupita-pitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.
15 Ndipo opitapitawo adzapitapita m'dziko, ndipo winaakaona pfupa la munthu aikepo cizindikilo, mpaka oikawo aliika m'cigwa ca unyinji wa Gogi.
16 Ndipo dzina la mudzi lidzakhala Hamona. Momwemo adzayeretsa dziko.
17 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani ku mbali zonse, kudza ku nsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikuru pa mapiri a Israyeli, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.