17 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani ku mbali zonse, kudza ku nsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikuru pa mapiri a Israyeli, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.
18 Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa ana a nkhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng'ombe, zonsezi zonenepa za ku Basana.
19 Ndipo mudzadya zonona mpaka mudzakhuta, ndi kumwa mwazi mpaka mudzaledzera za nsembe yanga ndakupherani.
20 Ndipo podyera panga mudzakhuta akavalo, ndi magareta, ndi anthu amphamvu, ndi anthu onse a nkhondo, ati Ambuye Yehova.
21 Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona ciweruzo canga ndacicita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira.
22 Ndipo nyumba ya Israyeli idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m'tsogolomo.
23 Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israyeli idalowa undende cifukwa ca mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.