1 Caka ca makumi awiri ndi zisanu ca undende wathu, poyamba caka, tsiku lakhumi lamwezi, caka cakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Mulungu linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.
2 M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israyeli, nandikhalitsa pa phiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mudzi kumwela,
3 Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ace ngati amkuwa, ndi cingwe cabwazi m'dzanja lace, ndi bango loyesa nalo, naima kucipata iye.
4 Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israyeli zonse uziona.
5 Ndipo taonani, panali linga kunja kwace kwa nyumba ya kacisi poizinga, ndi m'dzanja lace la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uli wonse mkono kudza cikhato; ndipo anayesa cimangidweco kucindikira kwace bango limodzi, ndi msinkhu wace bango limodzi.