10 Ndi zipinda za alonda za ku cipata ca kum'mawa ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, cakuno ndi cauko.
11 Ndipo anayesa kupingasa kwa cipata pakhoma pace mikono khumi, ndi utali wace wa cipata mikono khumi ndi itatu;
12 ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi cakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi cauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko.
13 Ndipo anayesa cipata kuyambira ku tsindwi la cipinda ca alonda cimodzi, kufikira ku tsindwi la cinzace, kupingasa kwace ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.
14 Anamanganso nsaaamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa cipata lidafikira kunsanamira.
15 Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la cipata kufikira khomo la khonde la cipata m'katimo ndiko mikono makumi asanu.
16 Ndipo panali mazenera a made okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa cipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, pa nsanamirazo panali akanjedza.