37 Ndi nsanamira zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.
38 Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi citseko cace; pamenepo anatsuka nsembe vopsereza.
39 Ndipo m'khonde la pacipata munali magome awiri cakuno, ndi magome awiri cauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula.
40 Ndi ku mbali yina ya khonde kunja, pakukwerera polowera pa cipata ca kumpoto, kunali magome awiri, ndi ku mbali inzace ya kucipata kunali magome awiri.
41 Magome anai cakuno, ndi magome anai cauko, ku mbali ya cipata; magome asanu ndi atatu, amene anapherapo nsembe.
42 Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m'litali mwace mkono ndi nusu, kupingasa kwace mkono ndi nusu, msinkhu wace mkono umodzi; pamenepo adafoika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera.
43 Ndi ziciri zangowe, cikhato m'litali mwace, zinamangika m'katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe.