11 Ndi pamadyerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.
12 Ndipo kalonga akapereka copereka caufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa cipata coloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, monga umo amacitira tsiku la Sabata; atatero aturuke; ndipo ataturuka, wina atseke pacipata.
13 Uziperekanso kwa Yehova mwana wa nkhosa wa caka cimodzi akhale nsembe yopsereza wopanda cirema, tsiku ndi tsiku, m'mawa ndi m'mawa, uzimpereka.
14 Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusanganiza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.
15 Momwemo apereke mwana wa nkhosa, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta, m'mawa ndi m'mawa, nsembe yopsereza kosalekeza.
16 Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wace wina wamwamuna mphatso idzakhala colowa cace, ndico cao cao ca ana ace, colowa cao.
17 Koma akapatsa mphatso yotenga ku colowa cace kwa wina wa anyamata ace, idzakhala yace mpaka caka ca ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma colowa cace cikhale ca ana ace.