3 Ndipo anthu a m'dziko alambire pa citseko ca cipata ici pamaso pa Yehova pamasabata, ndi pokhala mwezi.
4 Ndipo nsembe yopsereza imene kalonga azipereka kwa Yehova pa Sabata ndiyo ana a nkhosa asanu ndi mmodzi opanda cirema, ndi nkhosa yamphongo yopanda cirema,
5 ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini a wa mafuta wa paefa.
6 Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi ana a nkhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda cirema;
7 ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.
8 Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipata, naturuke njira yomweyo.
9 Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'madyerero oikika, iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumpoto kudzalambira, aturukire njira ya ku cipata ca kumwera; ndi iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumwera, aturukire njira ya ku cipata ca kumpoto; asabwerere njira ya cipata anadzeraco, koma aturukire m'tsogolo mwace.