6 Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi ana a nkhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda cirema;
7 ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.
8 Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipata, naturuke njira yomweyo.
9 Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'madyerero oikika, iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumpoto kudzalambira, aturukire njira ya ku cipata ca kumwera; ndi iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumwera, aturukire njira ya ku cipata ca kumpoto; asabwerere njira ya cipata anadzeraco, koma aturukire m'tsogolo mwace.
10 Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo poturuka iwo aturukire pamodzi.
11 Ndi pamadyerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.
12 Ndipo kalonga akapereka copereka caufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa cipata coloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, monga umo amacitira tsiku la Sabata; atatero aturuke; ndipo ataturuka, wina atseke pacipata.