1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku mapiri a Israyeli, uwanenere,
3 nunene, Mapiri a Israyeli inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu.
4 Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.
5 Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israyeli pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.
6 Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi nchito zanu zifafanizidwe.