4 Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.
5 Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israyeli pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.
6 Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi nchito zanu zifafanizidwe.
7 Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, matero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
8 Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwa amitundu pobalalitsidwa inu m'maiko maiko.
9 Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukila Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wacigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao acigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, cifukwa ca zoipa anazicita m'zonyansa zao zonse.
10 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanena cabe kuti ndidzawacitira coipa ici.