19 Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golidi wao cinthu codetsedwa; siliva wao ndi golidi wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi cokhumudwitsa ca mphulupulu zao.