12 ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aaigupto, adzati, Uyu ndi mkazi wace: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.
13 Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti cidzakhala cabwino ndi ine, cifukwa ca iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.
14 Ndipo panali pamene Abramu analowa m'Aigupto, Aaigupto anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri.
15 Ndipo akaronga ace a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwace kwa Farao.
16 Ndipo anamcitira Abramu bwino cifukwa ca iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi aburu akazi, ndi ngamila.
17 Koma Yehova anabvutitsa Farao ndi banja lace ndi nthenda zazikuru cifukwa ca Sarai mkazi wace wa Abramu,
18 Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nciani ici wandicitira ine? cifukwa canji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako?