14 Ndipo panali pamene Abramu analowa m'Aigupto, Aaigupto anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri.
15 Ndipo akaronga ace a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwace kwa Farao.
16 Ndipo anamcitira Abramu bwino cifukwa ca iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi aburu akazi, ndi ngamila.
17 Koma Yehova anabvutitsa Farao ndi banja lace ndi nthenda zazikuru cifukwa ca Sarai mkazi wace wa Abramu,
18 Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nciani ici wandicitira ine? cifukwa canji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako?
19 Cifukwa canji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nucoke.
20 Ndipo Farao analamulira anthu ace za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wace ndi zonse anali nazo.