18 Ndipo Melikizedeke mfumu ya ku Salemu, anaturuka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkurukuru.
19 Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkurukuru, mwini kumwamba ndi dziko lapansi;
20 ayamikike Mulungu Wamkurukuru amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
21 Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge cuma iwe wekha.
22 Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkurukuru, mwini kumwamba ndi dziko lapansi,
23 kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale cingwe ca nsapato, ngakhale kanthu kali konse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu;
24 koma cokhaci anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Aneri, Esikolo, ndi Mamre, iwo atenge gawo lao.