9 ndi Kedorelaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu ndi Amarafele mfumu ya Sinara, ndi Arioki mfumu ya Elasara; mafumu anai kugwirana ndi asanu.
10 Cigwa ca Sidimu cinali ndi zitengetenge tho; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.
11 Ndipo anatenga cuma conse ca Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka.
12 Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m'Sodomu, ndi cuma cace, namuka.
13 Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Mhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre M-amori, mkuru wace wa Esakolo, ndi mkuru wace wa Aneri; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
14 Pamene anamva Abramu kuti mphwace anagwidwa, anaturuka natsogolera anyamata ace opangika, obadwa kunyumba kwace, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kutikira ku Dani.
15 Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ace, nawakantha, nawapitikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.