1 Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamre, pamene anakhala pa khomo la hema wace pakutentha dzuwa.
2 Ndipo anatukula maso ace, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pace; pamene anaona iwo, anawathamangira kucoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
3 Mbuyanga, ngatitu ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu;
4 nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;
5 ndipo ndidzatenga cakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, cifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Cita comweco monga momwe wanena.
6 Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wace kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.
7 Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.