29 Ndipo ananenanso kwa iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi anai.
30 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzacita.
31 Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi awiri.
32 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwakhumim'menemo: Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca khumi.
33 Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwace.