5 ndipo ndidzatenga cakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, cifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Cita comweco monga momwe wanena.
6 Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wace kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.
7 Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.
8 Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng'ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya.
9 Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo.
10 Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yace; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pace.
11 Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, ana pitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumacita ndi akazi;