13 Taonani, ine ndiima pa citsime ca madzi; ndipo ana akazi a m'mudzi aturuka kudzatunga madzi;
14 ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo cotero ndidzadziwa kuti mwamcitira mbuyanga ufulu.
15 Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anaturuka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwace wa Abrahamu, ndi mtsuko wace paphewa pace.
16 Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ace, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wace, nakwera.
17 Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako.
18 Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m'manja mwace namwetsa iye.
19 Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse.